Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 98
Paphata pa Chichewa
Kodyakokha: Mkazi wosakwatiwa, mbeta.
Chitsanzo: (a) Tabwera kwanu kuno chifukwa tamva zoti
kuli kodya kokha. (2) Makolo amada nkhawa, anyamata
akamapanda kuzungulirazungulira pakhomo pamwe pali
kodya kokha.
Koka fodya: Kusuta fodya.
Chitsanzo: Amisala ambiri omwe ali m’taunimu anayamba
kukoka fodya wamkulu atauzidwa kuti amapatsa nzeru.
Koka mtima: Kukusangalatsa n’kufika potengeka nayo.
Chitsanzo: Nyimboyi yandikoka mtima.
Koka mtsonyo: Kutsonya, kuchita mwano.
Chitsanzo: Mayi ophika mowa aja amadziwa kuukoka
mtsonyo.
Koka utsi: Suta fodya.
Chitsanzo: Munthu amene amakoka utsi sasowa.
Kokera kwako: Kuchita kapena kunena chinthu kuti
chikuyendere bwino kuposa anzako.
Chitsanzo: Achuma ambiri ndi adyera, amangokokera
kwawo.
Kokomeza nkhani: Kuwonjezera zina ndi zina munkhani.
Chitsanzo: Amanena kuti mmene anadera, ayenera kuti
amamva kupweteka. Koma ine ndimaona kuti akokomeza
nkhani.
Kola chona: Kupalamula.
Chitsanzo: Ukapitiriza zimenezi ukola chona.
Kolola:
(a) Kukutengera ndalama zonse.
97