Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 97
Paphata pa Chichewa
Khwasula m’kamwa: Dyera nyama.
Chitsanzo: Madzulo ano tikhwasula m’kamwa.
Khwasula: Kutsinkha ndiwo.
Chitsanzo: Anawa akungokhwasula ndiwo.
Khwenya: Kudya mango akupsa popanda mpeni.
Chitsanzo: M’nthawi ya njala timapulumukira
kukhwenya.
Khwima m’manja: Kuzolowera kugwira ntchito zovuta.
Chitsanzo: Ntchito zake zikufuna anthu okhwima m’man-
ja.
Khwimbi la anthu (namtindi wa anthu, fumbi, khamu
la mnzanga ali pati, khamu la mundipondera mwana):
Anthu osawerengeka, anthu ambiri.
Chitsanzo: Kumaliroko kunali khwimbi la anthu/namtindi
wa anthu/fumbi/khamu la mnzanga ali pati/khamu la
mundipondera mwana.
Khwinthi: Kususuka.
Chitsanzo: Mwanayu ndi wakhwinthi.
Kiyama: Zoopsa. Mawu amenewa anayamba chifukwa
cha mawu omwe achisilamu amagwiritsa ntchito ponena
za mapeto a dzikoli.
Chitsanzo: Mukamanditengera maso m’mwamba,
ndikuonetsani kiyama.
Kodi mumaweta akalulu? Mawu amene amanenedwa
moseka, ponyoza munthu amene wagula masamba ambiri
oti akaphike kunyumba kwake.
Chitsanzo: Ndimadabwa kuti kodi mumaweta akalulu?
Masamba onsewa ndi a chiyani?
96