Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 94

Paphata pa Chichewa (2) Anthu ankadana aja pano ali khethekhethe. (b) Kuyang’ana mophethiraphethira. Chitsanzo: Atamuwaza mbamalo amangoti khethekhethe. Khofi: (a) Chibakera. Chitsanzo: Anamupatsa khofi. (b) Mtundu wa chakumwa chokhala ngati tiyi chomwe chimakhala chakuda komanso chowawa. Chitsanzo: Ndikufuna kumwa khofi. Kholophethe: Kubereka kwambiri, zambiri. Chitsanzo: (1) Mango angoti kholophethe m’mitengo. (2) Zi- patso pakhomo pawo zangoti kholophethe. Khoma malata m’mutu: Kukhala ndi dazi. Chitsanzo: Ana ambiri a masiku ano sakumachedwa ku- khoma malata m’mutu. Khoma ndawala: Kuyenda mofulumira kwambiri. Chitsanzo: Ndakumana nawo ataikhoma ndawala. Khomera kudowa: Kukhala wosabereka. Chitsanzo: Akuti asiyana ndi amuna awo chifukwa ana- khomera kudowa. Khonyola: (a) Kuvulaza. Chitsanzo: Akadzakuuza kuti unyamule mwanayu udzamugwire bwino kuopera kuti ukhoza kudzamu- khonyola. (b) Kuthyola Chitsanzo: Ndamuona akukhonyola chimanga. 93