Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 93

Paphata pa Chichewa Khalira khuthe: Kukhala pamavuto. Chitsanzo: Anthuwa akukhalira khuthe. Khalira m’phanthi: Khala mozunzika. Chitsanzo: Ukakhala mkamwini, umangokhalira m’phanthi. Khalukhalu: Utangokhala pang’ono. Chitsanzo: Khalukhalu, tinangoona atulukira! Khambi: Kusafuna kumvera, ena amati liuma. Chitsanzo: M’tauni muno simufuna munthu wakhambi, akhoza kulisiya dzikoli ndithu. Khamitsa mate (malovu): Kufunsa mafunso mosalekeza. Chitsanzo: Pakhomo pano pakabwera a Mboni ndi- wakhamitsa malovu. Khapa mtengo: Tchaja mtengo wokwera kwambiri. Chitsanzo: Mukapanda kuchenjera akukhapani chimtengo chodula. Khatcha mbama: Menya mbama. Mawu achipongwe ko- manso okokomeza onena za munthu akamenya mnzake mbama. Chitsanzo: Ndinawaona aphunzitsi akumukhatcha mbama. Khaulitsa: Lapitsa, kumvetsa wina kupweteka. Chitsanzo: Wakubayo anamukhaulitsa pomusenzetsa katundu yemwe anabayo. Khethekhethe: (a) Kugwirizana kwambiri. Chitsanzo: (1) Panopa aboma komanso azipembedzo ali khethekhethe. 92