Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 92

Paphata pa Chichewa unamuuza ndiye mumati wazikolokota kapena mungamutchule munthuyo kuti kazikolokota. Chitsanzo: Ndinamuuzatu nkhani yonse bwinobwino, koma wakanenena zina. Kazikolokota ameneyu! Kazinga bodza: Kunama. Chitsanzo: Ndinawapeza akulikazinga bodza. Kazitape (kazitule): Munthu wamiseche yemwe amati akamva nkhani uku, amazinyamula n’kukazikhuthura kwina. Angatanthauzeno munthu wodanitsa. Chitsanzo: Pamudzi pano pachuluka akazitape. Khala la moto: Vuto. Chitsanzo: Achimwene awo anangowakalasulira makala amoto n’kuthawa. Khala pachitsa: Khala wosabereka. Chitsanzo: Bambo ajatu anakhala pachitsa. Khala pampemphenu: Kukhala pamavuto. Chitsanzo: Anzanu ajatu akhala pampemphenu. Khala tsonga: (a) Kuchira pobereka mwana. Chitsanzo: Mayi anali ndi pakati uja wakhala tsonga. (b) Kukhala pansi bwinobwino. Chitsanzo: Pasapezeke wogona, aliyense akhale tsonga. Khala: Munthu wakuda bii. Chitsanzo: Mkwatiyu ndi khala. Khalani omasuka: Musachite manyazi kapena kumangi- ka. Chitsanzo: Khalani omasuka, mpakwanu pano. 91