Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 91

Paphata pa Chichewa Katapira: Kubwereka ndalama yoti udzabweza ndi chiwongola dzanja chochuluka. Chitsanzo: Awalanda nyumba chifukwa cha katapira. Katulutulu: Matenda otukusira omwe amakonda kugwira dzala. Chitsanzo: Chala chawo chinaduka atadwala katulutulu. Katundu: (a) Ali ndi mzeru zoopsa. Chitsanzo: Amene uja ndi katundu. (b) Munthu wolemera. Chitsanzo: Wagulanso galimoto ina, amene uja ndi katundu. Kaunjika: Zovala zogulitsidwa pamulu monga za m’mabelo. Chitsanzo: Ndimakonda kugula zovala za pa kaunjika chifukwa zimatchipa. Kavuuleluzi: Munthu wotsika. Chitsanzo: Amatuma akavuuleluzife. Kudzitsira: Kusampha mthupi. Chitsanzo: Ndikubwera kaye ndikadzitsire. Kavuwevuwe: Munthu wodanitsa, munthu wabodza, wamiseche. Chitsanzo: Pamudzi pano pachuluka akavuwevuwe. Kawawa: Mawu omwe amanenedwa potamanda chinthu kuti ndi chabwino kwambiri. Chitsanzo: Nsapato imeneyi ndi kawawa. Kazikolokota: Mawu amenewa amanenedwa pofotokoza kuti munthu wina wanena zosiyana ndi zimene 90