Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 90

Paphata pa Chichewa Kapitawo: Munthu wosabereka. Chitsanzo: Amene ajatu ndi akapitawo, ntchito yawo ndi kulondolera akazi awo aja basi. Kapolo: Munthu wovutika, wosauka, munthu yemwe amagwira ntchito koma osapeza kanthu. Chitsanzo: Unganene chiyani kapolo ngati iwe! Kapondam’zichiri: Munthu woyendayenda. Chitsanzo: Usadzayerekeze kukwatiwa ndi kapondam’zichitiri. Udzangokhala mulonda wa nyumba yake. Kapsala: Munthu wakuba. Chitsanzo: (a) Pakampani pano sitikufuna kumasunga akapsala. (b) Kuti akapsala asakubere, umafunika kuika ndalama m’kabudula wamkati kapena mukhamisolo. Kapunthabuye: Munthu wosauka. Chitsanzo: Ndingawapatse chiyani kapunthabuye ngati ine! Kasiyagoli: Munthu amene amaba koma m’kuthawa mosadziwika bwino. Chitsanzo: Apolisi anakhwimitsa chitetezo atazindikira kuti munthu wina ndi kasiyagoli. Katakwe: Katswiri. Chitsanzo: (1) Amene uja ndi katakwe pa nkhani yokonza njinga. (2) Akazi anu aja ndi katakwe popeka bodza. Katangale: Kupereka ndalama kuti akuchitire zinazake. Chitsanzo: (1) Boma lalonjeza kuti lithana ndi anthu onse a katangale. (2) Kulemera kujatu ndi katangale! 89