Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 9

Paphata pa Chichewa Amubatha: Amugwira. Chitsanzo: Anamubatha ali ndi mkazi wamwini. Amudomola: Amuchotsa. Chitsanzo: Achimwene anuwa awadomola m’gulu lobwereketsa ngongole lija. Amukhumula: Anamubera, kumupusitsa. Chitsanzo: Madobadoba ena a m’tauni anamukhumula ndalama zake. Amukwangwanula: Kubera munthu. Chitsanzo: Amukwangwanula ndalama zonse. Amunamuna ogona chitseko chosatseka: Mwamuna weniweni, wamphamvu. Chitsanzo: Kumalola anthu ngati ife, amunamuna ogona chitseko chosatseka. Amuomba: Amubera. Tanthauzo lake lenileni ndi kugunda. Chitsanzo: Akuba amuomba ndalama zonse. Amupatsa phuli/phuga: Chichewa cha achinyamata chomwe chimatanthauza kuti amupatsa mimba. Chitsanzo: Mtsikana uja wapatsidwa phuli/phuga ndi aphunzitsi ake. Amupyera: Mawu achipongwe onena za munthu amene wagwidwa. Chitsanzo: Anamupyera akuba matimati m’munda wa agogo. Amwandionerapati: Anthu afupiafupi. Chitsanzo: Kodi unawaonapo Amwandionerapati? 8