Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 89

Paphata pa Chichewa Kanyanga pakhosi: Gwira mwamphamvu pakhosi. Chitsanzo: Amukhululukira ngongole yaikulu, koma iyeyo akukanyanga mnzake pakhosi chifukwa cha 50 kwacha. Kanyanga: Kuimba bwino kwambiri gitala. Chitsanzo: Mwanayu amakanyanga nsambo. Kanyimbi: Munthu wopanda mphamvu, munthu wonunkha. Chitsanzo: (1) Iwe ndi kanyimbi, ndikhozatu kukuphwasamula. (2) Ndisadzamuonenso kanyimbi uja pakhomo pano. Kanyumba komata: Kuchimbudzi. Chitsanzo: Apita kukanyumba komata. Kapado: Nkhumba. Chitsanzo: Analumbira kuti sadzadyanso kapado chifukwa amamuwenga. Kapalemoto: Kapolo Chitsanzo: Enafetu pamudzi paja ndi akapalemoto, satiwerengera mkomwe. Kapasule: Munthu wodanitsa. Chitsanzo: Ameneyu ndi kapasule. Kape: (a) Munthu wopusa. Chitsanzo: Bamboyu ndi kape. (b) Sefa wansungwi. Chitsanzo: Ndani wabwereka kape wathu. Kaphazilambi: Munthu yemwe amafalitsa mabodza. Chitsanzo: Tachionani chikaphazilambi ndi chimulomo chake chachikulucho! 88