Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 88

Paphata pa Chichewa (2) Ndinadziwa kuti bambowa ndi akangandiwamba nditawapezerera akumwa tiyi kubafa. (3) Amuna ena ndi akangandiwamba, amachita kulemba zizindikiro mu ufa. Kanjipiti: Munthu wamfupi kwambiri. Chitsanzo: Ukakhala kanjipiti sukalamba mwansanga. Umaona misana ya alangwani ikusanduka uta, iwe wako uli gwa! Kankha nthenga: Kutuma munthu. Chitsanzo: Mpofunika kukankha nthenga kwa a mfumu. Kankhira: Kunamizira munthu wina wosalakwa. Chitsanzo: Sikutitu mundikankhire ine, nkhaniyi sikundikhudza. Kansanzawira: Munthu wovala nsanza. Chitsanzo: Kukubwera a kansanzawira aja. Kanthu n’chala: Kuti munthu udziwe bwino zinazake pamafunika kuti ena akuuze bwinobwino. Chitsanzo: Ndikufuna ndimvetsetse, pajatu kanthu n’chala. Kanthu ndi khama: Kuti upeze zimene ukufuna umafunika kuchita khama. Chitsanzo: Sinditopa kumufunsira mwina andilola. Paja kanthu ndi khama, phwiti anakwatira njiwa. Kanyama kanji: Mawuwa amanenedwa munthu akakhala kuti sakudziwa za zinthu zinazake ndipo akufunsa kuti adziwe zambiri. Chitsanzo: Tabuleti ndi kanyama kanji? Kanyanga nsambo: Kuimba bwino gitala. Chitsanzo: Akati akanyange nsambo sungamudziwe. 87