Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 87

Paphata pa Chichewa Kana kali kutsaya: Kukana zimene uzidziwa kapena wachita. Chitsanzo: Ndalama zanu watenga ndi yemweyu, kungoti akukana kali kutsaya. Musecheni mumugwira nayo. Kana m’maso muli gwa: Kukana ukudziwapo kanthu, kukanitsitsa mopanda manyazi. Chitsanzo: Satana ananena kuti Yobu adzamukana Mulungu m’maso muli gwa. Kana moto: Kukanika kupsa. Chitsanzo: (1) Chikunichi chakana moto. (2) Nsimayi yakana moto. Kana poyera: Kukana pagulu. Chitsanzo: Mkazi wako akakukana poyera, umafunika kungomusiya kuti adziwe mmene umbeta umawawira. Kanda padazi: Kuputa munthu. Chitsanzo: (a) Angabwere pakhomo panga pano n’kumandikanda padazi? (2) Si bwino kumawakanda anzako padazi. Kandionamaso: Kuchita kanthu chifukwa cha kuonana. Chitsanzo: Ndikadapanda kukuitanani mukanandipatsa moni inu? Moni wanuyutu ndi wa kandionamaso. Kangalika: Kulimbikira. Chitsanzo: Mukakhala okangalika akukwezani pantchito. Kangandiwamba: Munthu womana kwambiri, waumbombo. Chitsanzo: (1) Amene uja ndi kangandiwamba, dzulo zathu timadyera limodzi, lero zake akudyera kuchipinda. 86