Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 85
Paphata pa Chichewa
Kalulu khonje (kaponda nazale): Mphaka. Mawu onena
mwachining’a omwe ena amagwiritsa ntchito ponena za
mphaka amene akufuna kumupanga ndiwo. Mawuwa
amakonda kugwiritsidwa ntchito ndi angoni.
Chitsanzo: Kodi unamulawapo kalulu khonje?
Kama:
(a) Bedi.
Chitsanzo: Ndidzakwatira ndikadzagula kama.
(b) Kukama chiweto kuti chitulutse mkaka.
Chitsanzo: Ndisadzayerekeze kukupeza ukukama mkaka.
(c) Kutengera munthu zinthu zambiri.
Chitsanzo: Akungofuna kundikama ndalama zanga.
Kamatewe: Munthu wamatewe.
Chitsanzo: Kamatewe uja wabweranso.
Kamathigidi: Munthu wamatekenya.
Chitsanzo: Kamathigidiyo asalowe m’nyumba muno.
Kamatule: Munthu wakuba.
Chitsanzo: Akamatule ambiri masiku ano akumabwera
atavala masuti. Ukamazindikira kuti akubera mumakhala
m’mbuyo mwa alendo.
Kamba anga mwala: Nkhani zina ndi zovuta kuzimvetsa.
Chitsanzo: Zina ukanenena abale! Kamba anga mwala
ndithu.
Kamba:
(a) Chakudya cha paulendo.
Chitsanzo: Ndanyamulako kamba kuti njala ikandiwawa
ndidye.
(b) Fulu.
Chitsanzo: Ndinakumana naye atanyamula kamba.
84