Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 84

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Kalanga ine! N’chifukwa chiyani wachita zime- nezi. Kalapsulapsu: Woyenda mozemba, mbava. Chitsanzo: Kalapsulapsu akadutsa pakhomo, chomwe chimatsala chimakhala choti walephera kuchinyamula. Kalavulagaga: Ntchito yowawa kwambiri. Chitsanzo: Walamulidwa kuti akagwire ntchito ya kalavulagaga. Kalawe: Mowa kapena phala lolawa asanayambe kulima. Chitsanzo: Tipatseni kaye kalawe, kuti tikayamba kulima tiziona bwinobwino pamene pakupita khasu kuopera tingadziteme. Kaliba: Mtsikana wovala bwino. Chitsanzo: Anyamata ambiri amakonda kuimba miluzi akaona kaliba. Kalikiliki: Kusakhazikika chifukwa chogwira ntchito, ku- chita khama, kutanganidwa. Chitsanzo: (1) Ndinapeza aliyense ali kalikiliki kukonzekera ulendo. (2) Aliyense ali kalikiliki kukonzekera mayeso. Kalionera: Kuchita zinthu moonera ena. Chitsanzo: Mwanayu ali ndi kalionera. Kalipokalipo: Chilipo chimene chikuchitika. Chitsanzo: Madzulo alionse akumachoka. Ndithu kali- pokalipo. Kalowam’malaya: Njala Chitsanzo: Ndikulephera kuona bwinobwino chifukwa kandilowa m’malaya. 83