Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 82

Paphata pa Chichewa Kadyaubwerere: Zinthu zokoma zoti ukadya umafuna utadyanso zina. Chitsanzo: Zakudya zomwe amagulitsa ndi kadyaub- werere. Kadzanja: Wakuba. Chitsanzo: (1) Muzisunga ndalama zanu pamalo abwino kuopera anthu a kadzanja. (2) Mwana wanuyu ndi wakadzanja. Kadzidzi: Munthu yemwe sakonda kugona usiku, munthu woyendayenda usiku. Chitsanzo: Pitani mukagone, enawa ndi akadzidzi. Kadziotche: Munthu wopanda mantha. Chitsanzo: Kudzudzula bwana kumafuna akadziotche ngati inu. Kadziwamwini: Aliyense amadziwa yekha. Chitsanzo: Zoti mowa wakukwana imakhala nkhani ya kadziwamwini. Kafanikhale: Munthu wolimba mtima. Chitsanzo: Anamuchenjezatu kuti pamene paja pamakhala achifwamba, koma iye uja wangokhala kafanikhale. Kafansiyanji: Munthu wosauka. Chitsanzo: Asungwana otukuka safuna kukwatiwa ndi kafansiyanji. Kafiide: Mkazi woyera kwambiri. Chitsanzo: Wafunsira kafiide. Kafula: Munthu wamfupi. Chitsanzo: Anati sangalembe ntchito kafula. 81