Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 81

Paphata pa Chichewa Kabanga: Mowa. Chitsanzo: Amakonda kumwa kabanga. Kabwerebwere: Munthu womangopitapita kwinakwake. Chitsanzo: (1) Uyu ndi kabwerebwere kundende kuno. (2) Sitifuna akabwerebwere pamudzi pano. Kabweremawa: Chinthu chosalimba. Chitsanzo: Usadzagule nsalu m’mashopu amene aja, zinthu zimene amagulitsa ndi za kabweremawa. Kacherezera kankhani: Kunena nkhani moti wina imuipire. Chitsanzo: Amafuna kuti ziwakomere, n’chifukwa chake anayamba kucherezera kankhani. Kadam’manja: Munthu wosauka kwambiri. Chitsanzo: Sindingakwatiwe ndi kadam’manja. Kadangoyenda: Mawu amenewa amanenedwa zikakhala kuti mkazi wokwatiwa sakutenga pakati. Chitsanzo: Ndimaganiza kuti pofika pano akhala ataima, koma ayi ndithu, kadangoyenda. Kadaulo: Munthu waluso kwambiri pantchito yake. Chitsanzo: Ameneyu ndi kadaulo wosema ziboliboli. Kadaundamadzi: Nsima. Chitsanzo: Ndigule nkhuni pansikapa kuti ndikaphike kandaundamadzi. Kaduka kachinangwa: Nsanje yaikulu. Chitsanzo: Sindingakhale pamudzi pa anthu a kaduka kachinangwa. 80