Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 79

Paphata pa Chichewa Jagalijagali: Kumangozungulirazungulira, kumangoyendayenda. Chitsanzo: (1) N’chifukwa chiyani mukungoti jagalijagali apa? (2) Sakhala pakhomo, amangoti jagalijagali. Japani: Zinthu zosalimba. Mawu amenewa anayamba chifukwa zinthu zambiri zimene zinkabwera m’dziko lino zinkachokera ku Japani ndipo zambiri zinkakhala zosalimba. Chitsanzo: Nsalu za masiku ano ndi za Japani. Jelekani: Kapu yaikulu. Chisanzo: Mwana ngati iweyo sangamalize chijelekani chimenechi. Jerezera nkhani: Kulankhula mokometsera kuti ena akopeke. Chitsanzo: Akayamba kuijerekeza nkhani, umatha kudziwa kuti mwana uyu angadzachite bwino ntchito ya utolankhani. Jijirijijiri: Kutanganidwa ndi zinthu. Chitsanzo: Mukawapeza ali jijirijijiri. Jijirika: Munthu woduduluka, kapena wotengeka ndi zinthu. Chitsanzo: Mwana wawo uja ndi wojijirika. Jiwa: Gwidwa ndi nyama yolusa. Chitsanzo: Mbuzi yanga yajiwa. Jomba: Kulephera kupita kwinakwake. Chitsanzo: (a) Akafuna kujomba kuntchito amangonamizira kudwala. 78