Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 77

Paphata pa Chichewa Imandimaliza: Imandisangalatsa. Chitsanzo: (1) Ndemanga imene anapereka inandimaliza kwabasi. (2) Mwana amene uja amandimaliza. Imba mwiyo: Kunena zinthu monyozera ndiponso mosatsimikiza. Chitsanzo: Akayamba kuimba mwiyo amakhala kuti akulipeka bodza. Imba ng’oma yowambawamba: Chita zinthu zimene mnzakoyonso amafuna. Chitsanzo: Atamufunsira anayankha mwamunayo kuti, “Mwaimba ng’oma yowambawamba.” Ipha mpola: Kupumula, kupitidwa mphepo ina. Chitsanzo: (1) Ndipite kunyanja kuti ndikaphe mpola. (2) Sindikufuna kumagwira ntchito yokhetsa thukuta ena akungopha mpola. Ipha tsogolo: Kuwononga mwayi womwe ukanakuthandiza m’tsogolo, kuwononga tsogolo. Chitsanzo: Aphunzitsi amene amagona ndi ana a sukulu, amakhala akuwaphera tsogolo lawo. Ipitsa: (a) Pereka mimba. Chitsanzo: Zikumveka kuti mwana wanuyu ndi amene waipitsa mtsikana uja. (b) Kuononga mbiri ya munthu wina. Chitsanzo: Ulendo anapita kumudzi uja anakatiipitsako. Ipsa n’kumbuyo komwe: Kuvutika kwambiri. Chitsanzo: Anzanu aja anapsa n’kumbuyo komwe akuba atawabera katundu yense. 76