Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 76
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Mwana wanu mukumuikira kumbuyoyu
adzakugalukirani tsiku lina.
Ili m’mazira: Mawuwa amakonda kunenedwa zikakhala
kut nkhani inayake ikanaganiziridwabe kapena ikakhala
kuti sinatuluke.
Chitsanzo: Akuboma akungoti nkhaniyi idakali m’mazira.
Kaya adzaticheukira liti.
Ili mkati: Mawuwa amanenedwa ndi munthu amene
akugwira ntchito kapena amene akuona anzake akugwira
ntchito. Anganenedwe pouza munthu kuti ali pakati
pogwira ntchitoyo kapena anawapeza akugwira ntchito.
Chitsanzo: Ndimaganiza kuti ndikawapeza asanayambe,
koma ndinapeza ili mkati.
Ima mutu: Kusowa chochita.
Chitsanzo: Ndilibe ndalama zolipirira njinga ndaonongayi,
moti mutu wanga waima. Kaya ndikaziba kuti ndalama
ine?
Ima nazo: Akaiyamba ndewu sagwirika, sathawa.
Chitsanzo: Ngakhale anamumenya ndi kuseri kwa
chikwanje, sanaimve moti nayenso anayamba
kudzipulumutsa zibakera. Mwana amene uja amaima
nazo zibakera.
Ima pachulu: Kulalatira.
Chitsanzo: Musayerekeze kuwaputa, akuimirani pachulu.
Ima: Tenga pakati.
Chitsanzo: Mayi akaima amafuna zakudya zachilendo
monga ziboda za nkhumba, dothi komanso amafuna
kumva fungo la dizilo.
75