Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 75

Paphata pa Chichewa Igwa apa: Mawuwa amakonda kunenedwa pamlandu pouza munthu kuti alipire chifukwa cha mlandu umene wapalamula. Chitsanzo: Zaonekeratu kuti unaba nzimbe ya eni ndi iwe. Igwa apa! nkhuku ziwiri. Igwa chagada: Lephera kotheratu. Chitanzo: Amayesa kuchita zinthu zosatheka, lero agwa chagada. Igwa nkhope: Kuchita manyazi. Chitsanzo: Atamutulukira kuti amanama, mnyamatayo anagwetsa nkhope. Ika pachidale: Pangitsa kuti munthu asowe pothawira. Chitsanzo: Lero sanauone mpira chifukwa otseka kumbuyo anamuika pachidale. Ika pakona: Kupanikiza munthu, kupangitsa kuti zinthu zisayendere bwino wina. Chitsanzo: (1) Zimene anena zija zatiika pakona. (2) Koma ndiye mwatiika pakonatu anzanufe. Ikakuona litsiro sikata: Mavuto akati akupanikize satherapo. Chitsanzo: Anthuni ndikukumana ndi mavuto ine! Zikungokhala ngati ndalumpha m’chiwaya n’kugwera pamoto. Ndithudi, ikakuona litsiro sikata. Ikidwa pampani: Kupanikizidwa moti sungathawe. Chitsanzo: Anasiya kuyendayenda masiku ano, akazi awo anawaika pampani. Ikira kumbuyo (ika kumbuyo): Kuteteza munthu, kumutchinjiriza. 74