Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 74

Paphata pa Chichewa Idya mankhwala: Kumwa mankhwala. Chitsanzo: Ndatopa ndi kudya mankhwala. Idya manyazi: Chita manyazi. Chitsanzo: Mwana wanu akatenga mimba mumadya manyazi. Idya matako agalu: Munthu woyendayenda. Chitsanzo: Ameneyutu sakhazikika, anadya matako agalu. Idya moto: (a) Chita bwino kwambiri. Chitsanzo: Atsikana ambiri omwe amadya moto pa maphunziro amakhala onyansa. (b) Kukwiya. Chitsanzo: Mtsikanayo atangomutukwana, mnyamatayo anadya moto. Idya mtedza wakhwangwala: Kuiwalaiwala. Chitsanzo: Aphunzitsi ankakumbukira chilichonse aja anadya mtedza wakhwangwala. Idya zotema ndi nkhwangwa: Kupeza zinthu movutikira. Chitsanzo: Ntchito yawathera, moti akudya zotema ndi nkhwangwa. Ifa mphuno: (a) Osalota kuti pano pali chakuti. Chitsanzo: Iyeyu ndi wakufa mphuno, zoona sakudziwa kuti akuyankhula nayeyo ndi m’bale wake. (b) Osamva fungo. Chitsanzo: Amene aja mphuno zawo ndi zakufa, fungo lili m’nyumba muja samalimvayi. 73