Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 72

Paphata pa Chichewa Gwira pakamwa: (a) Kudabwa Chitsanzo: Nditawapeza akuthyola chitseko ndinangogwira pakamwa. (b) Kubisa. Chitsanzo: Akakandifunsa ndikangogwira pakamwa. Gwira pakati: Thandiza. Chitsanzo: Mwana ameneyu akhoza kudzatigwira pakati m’tsogolo. Gwira pakhosi: Menya munthu, kanyanga pakhosi. Chitsanzo: Bwana wawo anawagwira pakhosi. Gwira pamimba: Thandiza. Chitsanzo: Munthu amene uja ndi amene anandigwira pamimba. Gwira tambala pakamwa: Kulawira. Chitsanzo: Kuti utunge madzi pachitsime chimene chija umafunika kugwira tambala pakamwa. Gwira thupi: (a) Zolowera, kupima. Chitsanzo: Mavuto anandigwira thupi. (b) Kukukhala, kukukwana. Chitsanzo: Ndikufuna kuvala malaya omwe amandigwira thupi. Gwirani chodyeransima: Mawu amene anthu amanena akamafuna kuti anzawo awapatse moni wa padzanja. Chodyeransimacho amakhala akunena dzanja. Chitsanzo: Mulipo inu! Gwirani chodyeransima. 71