Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 70

Paphata pa Chichewa (b) Munthu amene amanyengerera akazi n’cholinga choti achite nawo zopusa. Chitsanzo: Pamudzi pano sitisekerera a gwamula. Gwanda (shati): Kudula munthu manja kapena mikono. Chitsanzo: (1) Wakuba uja amupatsa gwanda. (2) Ukapitiriza moyo wakubawu anthu adzakugulira shati. Gwedeza mbina: Yenda moyerekedwa. Mawuwa amanenedwa makamaka kwa akazi. Chitsanzo: Mukumupatsa matama ndi inuyo, n’chifukwa chake akugwedeza mbina. Gwedeza mutu: Vomera. Chitsanzo: Ndimadana ndi munthu woti azingogwedezera mutu pa chilichonse. Gwera pamphuno: Kukumana ndi mavuto n’kusowa nawo chochita, kukumana ndi mavuto mwadzidzidzi. Chitsanzo: Mavutowa atigwera pamphuno. Gwerula nkhwanga n’chambuyo (chumba): Kukhala wosabereka. Chitsanzo: Bambo amene aja anagwerula (gulula) nkhwanga n’chambuyo. Gwerulana mano: Chotsana mano. Chitsanzo: Akawasiya osawaleletsa agwerulana mano. Gwetserana mumchenga: Kukambirana nkhani inayake, kuthetsa mkangano. Chitsanzo: Akufuna kuti tigwetserane mumchenga. Gwidiza: Meza. Chitsanzo: Ndamupeza akugwidiza thobwa lija. 69