Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 7

Paphata pa Chichewa Alibe 2 koloko: Wosachedwa kupsa mtima, munthu wovuta. Chitsanzo: Akazi awo alibe 2 koloko. Akhoza kukulalatirani ngati mutawaputa. Alibe khalidwe: Ali ndi khalidwe loipa. Angatanthauzenso munthu wopanda pabwino. Chitsanzo: Mwanayu alibe khalidwe. Alibe mnzake: Alibe munthu wopikisana naye. Chitsanzo: Mtsikanayu alibe mnzake pankhani yovina. Alibe nazo gashe: Alibe nazo ntchito. Chitsanzo: Zoti anthu akumunena, alibe nazo gashe. Bola zake zikuyenda. Alibe pabwino: Alibe pokomera, samathokoza. Chitsanzo: Munthu ameneyu alibe pabwino, ngakhale utamuthandiza bwanji sayamika. Alibe pogwira: Ali m’mavuto. Chitsanzo: Gogowa alibe pogwira, ana awo onse anatsikira kulichete. Alibiretu ngakhale 1 tambala: Alibe kalikonse, alibiretu ndalama. Chitsanzo: Amandiuza kuti alibiretu ngakhale 1 tambala. Koma titangosiyana, ndinawaona akugula tchipisi. Alungalunga: Opanda chilema. Chitsanzo: Wolumala uja anakwatiwa ndi munthu walungalunga. Amadya napondapo: Amaipitsa pamalo omwe wakhala. Chitsanzo: Mkamwiniyu amakhala ngati wabwino pamaso pa anthu, koma amadya napondapo. 6