Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 69

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Ndinamupeza akuguza njinga. Gwadausankhe: Zovala za kaunjika, pakaunjika. Chitsanzo: Ukafuna zovala zotchipa umafunika kupita pa gwadausankhe. Gwadira: Mawuwa amatanthauza kulemekeza, kupembedza kapena kutamanda chinachake. Koma angagwiritsidwenso ntchito mwanjira ina ngati munthu akufuna kuti wina avutike kaye kuti amuthandize. Chitsanzo: Akufuna ndizichita kuwagwadira (kuwapembedza) kuti andithandize? Gwadirani pamachika (gwadirani pachitsapo): Kuuza mlendo mwaulemu malo okhala. Chitsanzo: Takulandirani, mukhoza kugwadira pamachikapo. Gwagwagwa: Ali bwino, adakali ndi mphamvu. Chitsanzo: Akumwalira ndi ana, nkhalamba ija idakali gwagwagwa. Gwagwagwa: Mawuwa amanenedwa ponena za munthu amene adakali ndi mphamvu kapena sakudwala. Chitsanzo: Anawa ndi amene akudwaladwala, nkhalamba zili gwagwagwa. Gwala: Munthu waulesi amene safuna kugwira ntchito. Chitsanzo: Aliyense amafuna mkazi wotakataka, osati gwala ngati amene uja. Gwamula: (a) Khalidwe la munthu woipa. Chitsanzo: Mwamuona gwamula uja, chenjerani akudyerani ana. 68