Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 68

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Osamawayamba dala anthu angadzakugululeni mano. Gulula nkhongono (kuguluka nkhongono): Fooketsa, kufooka chifukwa cha zinazake zimene zachitika. Chitsanzo: (1) Zimene achitazi zandigulula nkhongono. (2) Ndangogulukiratu nkhongono. Gululu: Kukumana mosayembekezereka. Chitsanzo: Anangoti gululu ndi mkazi wachibwenziyo. Guma: Lephera. Chitsanzo: Anaponya bwino mwalawo, koma wachita guma. Gunata: Kupusa. Chitsanzo: Kugunata kwake kumeneku mungalemere inu? Gunda mgolo: Kupeza palibe kapena kulephera. Chitsanzo: (1) Ndinachedwa kudzuka, moti pamene ndimakafikako ndinagunda mgolo chifukwa ndinakawapeza kulibe. (2) Mayeso a chaka chino anali ovuta moti ana ambiri agunda mgolo. Gundana mitu: Kukambirana pa awiri. Chitsanzo: Kodi tingapite kaye poduka mphepo kuti tikagundane mitu? Gututu: Chitini kapena chinthu chimene anthu amakodzeramo usiku akamaopa kutuluka panja. Chitsanzo: Kodi mwalowetsa gututu? Guza: (a) Chofunda, bulangete. Chitsanzo: Amubera guza lake. (b) Kukankha chinthu. 67