Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 66
Paphata pa Chichewa
Gomo: Phiri.
Chitsanzo: Kumudzi kwawo ndi kumagomo.
Gona m’mankhokwe: Kukhala m’mavuto.
Chitsanzo: Mvula ikakuona litsiro sikata! Anzanu ajatu
mavuto sakuwachoka, akungogonera m’mankhokwe.
Gona ndi mwinikhutu yemwe: Kugona tulo tofa nato,
kugona kwambiri.
Chitsanzo: Ndinalowa m’nyumbamo. Koma zikuoneka kuti
agona ndi mwinikhutu yemwe.
Gona palumbe: Kugona osafunda kanthu.
Lumbe ndi mbalame yomwe imagona pamtetete popanda
chisa.
Chitsanzo: (a) Gombeza langa lanyowa, moti lero ndigona
palumbe. (b) Wakodzera wekha bulangete lako, lero ugona
palumbe.
Gona pathala: Kugona mosiyana malo m’banja chifukwa
choti wina akusamba kapena pakhomo pakagwa maliro.
Chitsanzo: Akangoona kansalu pakama, amadziwa kuti
afunika kumagona pathala.
Gona: Kupusa.
Chitsanzo: Sindifuna mwamuna wogona chonchi.
Gondola:
(a) Kupusa.
Chitsanzo: Munthu ameneyu ndi gondola.
(b) Chidengu chachikulu.
Chitsanzo: Mwanayu musamamusenzetse gondola.
Gonera banzi (mpunga kapena zakudya zina): Mawu
omwe anthu amanena modandaula kuti patsikulo
65