Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 65

Paphata pa Chichewa Gilibati: Mawu odyera omwe amatanthauza nkhumba. Chitsanzo: Lero tidyera Gilibati. Gitala: (a) Mphere. Chitsanzo: Gitala imayanja anthu auve. (b) Kudzikanda. Chitsanzo: Munthu amene ndinakhala naye pafupi amaimba gitala. Godomala (godyaomala): Kupusa. Chitsanzo: (a) Osamachita zinthu zogodolama chonchi, kumachenjerako. (b) Chamba ndi chimene chinachititsa kuti agodomale. Gogodera: (a) Kuyankhula zambiri za chinachake ndi kuwonjezera bodza. Chitsanzo: Malume analigogodera bodza, pofuna kukopa munthuyo kuti awagule mbuzi yawo. (b) Kunyindilira, kuyesetsa kuti zinazake ziyende kapena kuti zitheke. Chitsanzo: Tipita kuti tikagogodere. Mwina angakatilole. Gogometsa: Thamangitsa. Chitsanzo: (1) Atamutulukira kuti ndi wakuba, anayamba kumugogometsa. (2) Mukamakachita matukutuku akakugogometsaniko. Gombeza: Bulangete, guza, chofunda. Chitsanzo: Amubera gombeza lake. Gombeza: Bulangete. Chitsanzo: Juni asanayambe kulavula, mpofunika ndigule gombeza. 64