Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 64

Paphata pa Chichewa Gambalagambala: (a) Kungoti balalabalala, mbwee. Chitsanzo: Mitembo inangoti gambalagambala. (b) Kumvekedwe ka kugwa pansi kwa chinthu. Chitsanzo: Chitinicho chitagwa chimangoti gambalagambala! Ganda makande: Kuyenda wapansi. Chitsanzo: Ndinalibe ndalama moti ndinangoganda makande. Ganda: (a) Nyama ya nkhumba. Chitsanzo: Ndagulako ganda kuti ana akaimbe lokoma kunyumbaku. (b) Chikopa. Chitsanzo: Chotsani gandalo. Gangidwa: Kumenyedwa koopsa. Chitsanzo: Usadzayambanenso ndi amene uja, angadzakugange tsiku lina. Gemu yagona: Zavuta, zalephereka. Chitsanzo: Nditaona kuti wabwerera, ndinangodziwa kuti gemu yagona. Genda kudambwe: Kupalamula. Chitsanzo: Amakana kupita kumudzi chifukwa anagedwa kudambwe. Geya mwano: Kuyankhula chipongwe chachikulu. Chitsanzo: (1) Mwanayu wayamba kuugeya mwano. (2) Ana a masiku ano akumaugeya mwano. 63