Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 63

Paphata pa Chichewa Gadama: Lephera. Chitsanzo: Iye ankalimbikira koma atalemba mayeso anagadama. Gaga: (a) Deya. Chitsanzo: Tigulitseni gaga. (b) Ufa, chakudya. Chitsanzo: (1) Tinagona nayo chifukwa tilibe gaga. (2) Bola chaka chino mvula igwe bwino kuti tisadzasowe gaga. Gagada: (a) Luma. Chitsanzo: Wamisalayo anagagada chala cha munthu ankamulozayo. (b) Menya koopsa. Chitsanzo: Anzanu aja awagagada anzawo kumowa. (c) Khapa, kapena kuswa chinthu. Chitsanzo: Tagagadani maunguwo. Galika (tswalika): Kumeza chonse. Chitsanzo: Nditamupempha anangogalika chonse. Galu: Munthu wopanda pabwino. Chitsanzo: (1) Mwamuna ameneyu ndi galu! (2) Kodi galu uja walowera kuti? Galuwakuda: Njala. Chitsanzo: Pakhomo paja padutsa galuwakuda. Gamazula: Mowa wowawa kwambiri. Chitsanzo: Munthu akamamwa gamazula, amaipitsa nkhope. 62