Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 62
Paphata pa Chichewa
(b) Kutha ntchito, kukalamba.
Chitsanzo: Ife ndiye tafumbwa, ntchito zinazi tisiyire
anyamatanu.
Fumuka: Kuchoka pamalo.
Chitsanzo: Ndabwera lija ndi kale, tsopano ndifumukepo.
Funda khofi: Kugona osafunda.
Chitsanzo: Wakodzera zofuna zako, lero ufunda khofi.
Funda mbiya: Pusa.
Chitsanzo: Akanakhala wofunda mbiya akanalephera.
Funda phale: Kupepera, kumbwambwana, kupusa.
Chitsanzo: Sindingamagwire ntchito ndi anthu ofunda
phale.
Fundika bulangete: Pusitsa.
Chitsanzo: Mukapusa akufunikani bulangete.
Funsa ngati kupolisi: Kufunsa mafunso mosalekeza.
Chitsanzo: Osandifunsa ngati kupolisi! Ngati mukufuna
kudziwa zonse bwanji osangopita komweko?
Fwichirira:
(a) Kusaoneka bwino, kutuwa.
Chitsanzo: Afwichiriramotu m’taunimu.
(b) Kusuta kwambiri fodya.
Chitsanzo: Musadzabwerenso ndi anzanu ofwichirira
mapapo aja.
Fwifwa:
(a) Kutha ntchito
Chitsanzo: Mfundo za m’Baibulo sizifwifwa.
(b) Kusaoneka bwino.
Chitsanzo: Sindingavale zovala zofwifwa.
61