Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 60

Paphata pa Chichewa Fodya: Opusa. Chitsanzo: Bambo amene aja ndi afodya. Fola pamzere: Kukhala pamzere. Chitsanzo: Amene akufuna kulandira phala akafole pamzere. Fota: Kudikira mpaka kutopa. Chitsanzo: Tinadikirira mpaka kufota. Fudugu: Kudzikweza, kudzimva. Chitsanzo: Ndidamupeza ali fudugu, mapewa ali m’mwamba. Fudyama: Kupusa. Chitsanzo: Anthu ambiri ofudyama amakhala achipongwe. Fufuta m’manja: Lephera. Chitsanzo: Ndimaganiza kuti nanenso ndidya nawo ndalamazo, koma ndinangofufuta m’manja. Fuka nthunzi: Kupusa. Chitsanzo: Anamusiya akungofuka nthunzi. Fukula: (a) Ulula zomwe zinabisidwa. Chitsanzo: Atangomangidwa, apolisi anafukula milandu yawo yonse. (b) Kuuza ena zokhuza munthu monga mmene wakhala ukumuthandizira kapena zoipa zimene amachita. Chitsanzo: Mwati mutifukule chifukwa mwatithandiza! Fula: (a) Kuchotsa chiwalo choberekera. Chitsanzo: Anthu onse omwe amagwira ntchito kwa 59