Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 6

Paphata pa Chichewa Ali mafupa okhaokha: Waonda kwambiri. Chitsanzo: Malume anu angotsala mafupa okhaokha. Ali mutu gwa: Mawuwa amanenedwa monyoza kwa munthu wosamva. Chitsanzo: Tamuoneni, ali mutu gwa ngati sakumva! Ali ndi mano achipani: Ali ndi mano achikasu, ali ndi chiseyeye. Mawu amenewa anayamba chifukwa cha mtundu womwe chipani cha UDF chinkagwiritsa ntchito. Ndiye ponena monyoza za munthu yemwe mano ake ndi achikasu, ankangoti ali ndi mano achipani. Chitsanzo: Atangomwetulira mpamene ndinadziwa kuti ali ndi mano achipani. Ali ndi mfundo: Amayankhula zomveka, amanena zanzeru. Chitsanzo: Mwanayu ali ndi mfundo. Ali ndi mtima: Amene akundifunabe, amene wandikonda. Chitsanzo: Amene ali ndi mtima anditsate. Ali ndi mwana agwiritse: Zafika povuta, mpofunika kuchita khama, kulimba nazo. Chitsanzo: Zafikapa, ali ndi mwana agwiritse! Ali ndi thupi: Ndi wonenepa. Chitsanzo: Akazi awo ali ndi thupi. Ali ndi ziwindi: Ndi wamakani. Chitsanzo: Mwanayu ali ndi ziwindi. Ali pabwino: Zinthu zikuwayendera. Chitsanzo: Anzathuwa ali pabwino, zawo zikuwayendera. 5