Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 59

Paphata pa Chichewa Felemu ndi chitseko: Anthu ogwirizana kwambiri. Chitsanzo: Anthu amenewa ndi felemu ndi chitseko. Fera m’chipanda: Kumwa mowa moipa, kumwa mowa kwambiri. Chitsanzo: Malume anuwa adzafera m’chipanda. Amakonda kumwa osadyera. Fera m’mazira: Kutha zisanadziwike, kulephereka. Chitsanzo: Boma linkati litipatsa chipukuta misozi, koma zinangofera m’mazira. Fera za eni: Kuzunzika pankhani za ena. Chitsanzo: Analakwa ndi atsibweni anthu, ife tikungofera za eni. Finya munthu: Menya munthu, kwenya munthu mwamphanvu. Chitsanzo: Anzakewo anamufinya. Fisi: (a) Munthu wamantha. Chitsanzo: Osamakhala ngati munthu wamkazi iyayi, kumangochita mantha ndi chilichonse! Inutu ndi fisi. (b) Munthu wankhuli (nkhwiru). Chitsanzo: Pamudzi pano pachuluka afisi, amadya chilichonse ndi apusi omwe, ndipo nyama ikaola sataya. (c) Munthu amene ena amapeza kuti awaberekere mwana. Chitsanzo: Inutu zakukanikani, mpofunika m’nyumbamu tilowetsemo fisi. Fodya wamkulu: Chamba. Chitanzo: Ana ena a sukulu akumasuta fodya wamkulu. 58