Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 58

Paphata pa Chichewa Dzuwa likuswa mtengo: Masanasana. Chitsanzo: Amaba chimanga dzuwa likuswa mtengo. Dzuwa likuwamba mtengo: Masanasana. Chitsanzo: Amaba chimanga dzuwa likuwamba mtengo. Dzuwa lipepe: Dzuwa lichepeko mphamvu. Chitsanzo: Ndinyamuka, ndikudikira kuti dzuwa lipepe. Dzuwa: (a) Chilala, njala. Chitsanzo: Chaka chino m’dziko muno muli dzuwa. (b) Pamavuto Chitsanzo: (1) Si bwino kusiya mnzako akakhala padzuwa. (2) Bamboyo analithawa banja lake n’kulisiya liri padzuwa ataona kuti mimba zoti adyetse zachuluka. 57