Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 56

Paphata pa Chichewa nkhaniyi yandidzera kunkhongo? Dziko lidakali mphonje: Kalekale zinthu zisanasinthe mmene zilili masiku ano. Dziko lidakali losiyana ndi limene lili pano. Chitsanzo: Padangotero! Kalekalelo dziko lidakali mphonje, kunali kalulu ndi fisi. Dziko lidzatha: N’kosatheka kapena n’zokayikitsa. Mawuwa anganenedwe ponena kuti zinazake zitachitika, dziko likhoza kutha. Chitsanzo: Sangabwere kuno amene uja. Akadzabwera dziko lidzatha. Dziko likali nsoka: Kalekale zinthu zisanasinthe mmene zilili masiku ano. Chitsanzo: Zimenezi zinachitika dziko likali nsoka. Dziko: Anthu. Chitsanzo: Atakana kukachita maphunziro apamwamba kunja, dziko linadabwa naye kwambiri. Dziko: Manda. Mawu amenewa amagwiritsidwa ntchito kuti ana asadziwe kumene mumakaika munthu akafa. M’buyomu ana ankatsekeredwa m’nyumba pakhomo pakachitika maliro ndipo sankaloledwa kupita kumanda chifukwa cha zikhulupiriro zina. Chitsanzo: Mpofunika tipite kudziko kuti ndikakuonetseni pomwe m’bale wanu anagona. Dzimverem’tolo: Mawuwa amanenedwa pofuna kutsindika mfundo yakuti munthuyo wadzimvera yekha. Chitsanzo: Apatu ndiye dzimveremtolo, musiye khalidwe loipali. 55