Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 53

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Malitera wapeza duwa. Duziduzi: Kuyenda limodzi, kuyenda shosholo. Chitsanzo: Ndinawaona akuyenda duziduzi. Dwachedwache: Kuchita zinthu movutikira, kuchita zinthu mosalongosoka. Chitsanzo: (1) Zochita za munthu ameneyu ndi zadwachedwache. (2) Amangoyenda mwadwachedwache. Dwachedwache: Wosakhulupirika kwenikweni, tambwali. Chitsanzo: Sindimafuna mwamuna wa dwachedwache. Dwala: Funitsitsa kwambiri. Chitsanzo: Ndikuwadwala kwambiri makolo anga. Dyabolosi: Munthu woipa kwambiri. Mawuwa amapezeka m’Baibulo ndipo anachokera kuchigiriki. Amatanthauza Satana. Chitsanzo: Ndiwe dyabolosi eti. Dyera mapilitsi: Dyera nandolo, nyemba, sawawa kapena ndiwo zina za m’gulu limeneli. Chitsanzo: Ndikagule kanyenya kuti ndipumeko kudya mapilitsi. Dyera mpamba (kudya mpamba): Kudyera ndalama za geni. Chitsanzo: Ukadyera mpamba umavutika koopsa. Dyera nthambo: Kudyera matumbo. Chitsanzo: Akaphika nkhuku amakonda kunena kuti ana adyera nthambo. Dyera pinto: Kudyera mutu wa nkhuku. Chitsanzo: Anawanamiza anawa kuti akamakonda kudyera pinto adzakhala anzeru kwambiri. 52