Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 51

Paphata pa Chichewa (2) Ameneyu ndi dolo wa galimoto. (b) Munthu wautambwali yemwe amafuna kupusitsa ena. Chitsanzo: M’taunimu mwachuluka madolo. Dongolera: Kuchita zinthu zofunika, kuchita chinachake mwanjira yabwino kwambiri. Chitsanzo: Apa ndiye mwaidongoleratu, mpaka kuphikiratu nsima! Dontha: Kupusa. Chitsanzo: Mtsikana amene uja ndi wodontha. Dothi lokhalokha: Ambiri. Chitsanzo: Kumsonkhanoko kunali dothi lokhalokha. Dothi: Zochuluka. Chitsanzo: Kumaliroko galimoto zinali dothi. Dovu: Amatanthauza nkhuli. Chitsanzo: Munthu wadovu sasangalala mukamuphikira chitambe. Duduluka: Kutengeka ndi zinthu. Chitsanzo: Pakampani pano sitifuna anthu oduduluka. Duka mikono: Kusowa chochita. Chitsanzo: Vutoli latidula mikono. Duka nzengo: Wamakhalidwe amphulupulu. Chitsanzo: Mwana amene uja anaduka nzengo, sati wapalamula liti. Dula apa: Munthu woyendayenda. Chitsanzo: Munthu akakhala dula apa sachedwa kukumana ndi mavuto. Dula mwana (tsempha): Kuchita chiwerewere mwana wako ali m’chilowero kapena m’chikuta. Malinga 50