Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 50

Paphata pa Chichewa kuwajeda, koma anadzidzimuka ataona mwini wakeyo diso lili biriwiri. (2) Pamene ankamutengera nkhuku zake, diso lake linali liri biriwiri. Diso lili pamtunda: (a) Munthu yemwe akuoneka mwankhawa. Chitsanzo: Pamene amabwera n’kuti diso lili pamtunda. (b) Akufuna kufa. Chitsanzo: Tinawapeza atagwa pansi, diso lili pamtunda. Mbatata ndi imene inawathimba pakhosi. Diso lili piriwiri: Atatulutsa diso, maso atafiira. Chitsanzo: (1) Mmene amafika kunyumba n’kuti diso lili piriwiri. (2) Maso ake ali piriwiri ngati wasuta chamba. Diso limodzi: Kuona pang’ono. Chitsanzo: Alendo ajatu ndinangowaona diso limodzi. Doda chikopa: Kumenya bwino mpira. Chitsanzo: Anyamata a timu imeneyi amadoda chikopa. Dodoma: (a) Kuchita chibwibwi. Chitsanzo: Amawerenga mododoma chifukwa cha mantha. (b) Kudabwa. Chitsanzo: Ndinadodoma nditawaona ali mimba pamtunda. Dokodoko (nokonoko): Kuda, uve, litsiro. Chitsanzo: (1) Zovala zawo zinali zadokodoko. (2) Pakhomo pawo ali ana a nokonoko. Dolo: (a) Katswiri. Chitsanzo: (1) Amene uja ndi dolo pa nkhani ya mpira. 49