Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 5

Paphata pa Chichewa Akuka: Apongozi. Chitsanzo: Kunyumba kwabwera akuka anga. Akukupondererani: Akukuposani. Chitsanzo: Mwanayutu akukupondererani m’kalasi muno. Akuluakulu n’kudzala: Akuluakulu ndi amene amathetsa nkhani. Nkhani iliyonse imakathera kwa iwowo. Chitsanzo: Tabwera kwa inu chifukwa tikudziwa kuti akuluakulu n’kudzala. Akunjira: Alendo. Chitsanzo: Akunjira, takulandirani! Akupeza bwino: Achira. Chitsanzo: Amadwala aja tsopano akupeza bwino. Akusowa pogwira: Akuvutika kwambiri. Chitsanzo: Amene sanakolole chaka chatha akusowa pogwira. Ali chabe: Alibe kanthu, ali chimanjamanja. Chitsanzo: Angobwerako ali chabe. Ali m’dothi: Kugwa kwambiri (kuphofomoka) Chitsanzo: Mnzakeyo anachipulumutsa chibakera, ndipo ndinangoona ali m’dothi. Ali m’madzi: Ali m’mavuto, akumana nazo. Chitsanzo: Akangomugwira ali m’madzi. Ali m’maso: (a) Asanagone. Chitsanzo: Mukamadzabwera mudzandipeza ndili m’maso. (b) Asanamwalire. Chitsanzo: Mukanabwera dzulo mukanawapeza ali m’maso. Atisiya m’mawa womwewu. 4