Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 49

Paphata pa Chichewa Dambolachepa: Gwape, nangwale. Chitsanzo: Ndani angakwanitse kugwira dambo lachepa? Dedera: Kuchita mantha mwinanso kuyamba chibwibwi. Chitsanzo: Anayamba kudedera atakumana ndi apolisi. Delila: Mkazi wokhala ngati akukukonda koma akufuna kukupweteka, mkazi wachinyengo. Chitsanzo: Achuluka Adelila masiku ano. Dendebza: Nyamula mobisa. Chitsanzo: Munyamule modendebza kuopera ena angakuoneni. Dibwa: Kudyedwa. Chitsanzo: (1) Nsomba imeneyi imadibwa. (2) Chinthu chimenechi si chodibwa. Dindadinda: Zovala zothina kwambiri mpaka kumadinda zamkati. Chitsanzo: Abusa anakalipira anthu onse omwe anavala dindadinda patsikulo powauza kuti asiye kuchita malonda ndi matupi awo. Diso la nkhwezule: Kuyang’ana monyoza, mokwiya. Angatanthauzenso kuyang’ana munthu ndi mtima wofuna kumuwononga. Chitsanzo: Amandiyang’ana ngati akhoza kundicheka ndi maso awo. Nthawi zonse amandiyang’ana ndi diso la nkhwezule. Diso lili biriwiri: Ali pompo. Chitsanzo: (1) Amaganiza zoti achokapo, ndiye anayamba 48