Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 47

Paphata pa Chichewa Chokolo: M’zikhalidwe zina mwamuna akamwalira, m’bale wake amakwatira mkaziyo ngakhale ali kale ndi mkazi wina. Akatero timati mkaziyo walowa chokolo. Chitsanzo: Mkaziyu analowa chokolo mwamuna wake atatisiya. Chopangitsa malovu thethethe m’kamwa: Chakudya chokoma kwambiri. Chitsanzo: Azakhali anatiphikira chakudya chopangitsa malovu thethethe m’kamwa. Chophwamphwanthika: Chophwanyika, chafulati. Chitsanzo: Chigumu mwaphikachi ndi chophwam- phwanthika. Chophwathalala: Chopwanyika, chafulati, chodirizika. Chitsanzo: Wanyamula chitsulo chophwathalala. Chosakhala bwino: (a) Choipa. Chitsanzo: Khalidwe limene mwayambali ndi losakhala bwino. (b) Chakudya chosakoma kapena chowonongeka. Chitsanzo: Chakudyachi ndi chosakhala bwino. Chothyokathyoka: Chosamveka, chosalongosoka. Chitsanzo: Amayankhula Chichewa chothyokathyoka. Chotsa chimbenene: Kuchenjeretsa, kukhaulitsa, kumenyedwa, kugonjetsedwa koopsa. Chitsanzo: (a) Mnyamata woyerekedwa uja amuchotsa chimbenene. (b) Abwere kuno timuchotse chimbenene. Chotsa dalazi: Idya zankhuli. Chitsanzo: Tikagule mutu wa mbuzi kuti tichotseko dalazi. 46