Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 45

Paphata pa Chichewa (b) Munthu wovuta kwambiri, wosowetsa mtendere. Chitsanzo: Mwana wanuyu ndi chiwanda. Chiwerewere: Mkazi kapena mwamuna yemwe amagona ndi anthu ena kaya ali pabanja kapena ayi. Angagwirenso ntchito ponena za munthu yemwe wasiya mwamuna kapena mkazi wake n’kumakagona ndi anthu ena. Chitsanzo: Mwamuna ameneyu ndi wachiwerewere. Chiwongoladzanja: (a) Ndalama yoonjezera pamwamba pa ndalama imene un- abwereka kapena kukongola. Chitsanzo: Ngongoleyi ili ndi chiwongoladzanja chochulu- ka. (b) Ndalama yomwe munthu amapeza akasungitsa ndala- ma zake kubanki. Chitsanzo: Ndikanasungitsa ndalama zanga kubanki ndi- kanapeza chiwongoladzanja. Chizimalupsa: Mvula yoyambirira. Chitsanzo: Nyumba yawo inagwa ndi chizimalupsa. Chizimbwitsa mphoyo: Kuoneka ngati munthu wosadziwa kanthu pomwe ukudziwa bwinobwino nkhani yake. Chitsanzo: Anaotcha udzuwo ndi iyeyo koma atafika anayamba kuchita chizimbwitsa mphoyo. Chizumbazumba: Chizungulire. Chitsanzo: Ndikuchita chizumbazumba. Chizungulire: Kuona kuti zinthu ngati zikuzungulira. Chitsanzo: Ndikathamanga kwambiri ndimachita chizungulire. 44