Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 44

Paphata pa Chichewa chithunzithunzi cha nkhaniyi. (b) Chifaniziro chimene chimaoneka chinthu kapena munthu akaima padzuwa. Chitsanzo: Dzuwa likafika paliwombo, chithunzithunzi sichioneka. Chitsa chotsala mulupsa: Mawuwa amanena za chitsa chomwe chapulumuka pamene tchire limapsa. Angatanthauze munthu wamphamvu komanso wosatekeseka. Chitsanzo: Ameneyu ndi chitsa chotsala mulupsa. Chitseko ndi felemu: Kukhala ogwirizana kwambiri. Chitsanzo: Banja limeneli ndi chitseko ndi felemu. Chitserekwete: Munthu wopanda nzeru, wosamva, wosathandiza. Chitsanzo: Mwanayu ndi chitserekwete. Chitsirizira: Munthu womalizira kubadwa. Chitsanzo: Ine ndinadziwa kuti ndi chitsirizira nditaona zimene ankachita. Zikuoneka kuti anamulerera pachilolo. Chitsizi: Munthu wochita zoipa mochenjera kwambiri. Chitsanzo: Ana osamawasiya ndi chitsizi, akhoza kuwachita chipongwe. Chitsulo: Munthu wamphamvu. Chitsanzo: Ntchito imeneyi sikufunika munthu wa mafupa a mapesi, ikufunika chitsulo. Chiwanda: (a) Munthu woonda kwambiri. Chitsanzo: Mnyamata uja anadwala kwambiri moti wasanduka chiwanda. 43