Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 43

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Anthuwo atayamba kumuwowoza, anachita guni. Chita masamu: Peza nzeru, fufuza choti uchite. Chitsanzo: (1) Wayamba kupanga masamu kuti apeze chonamizira. (2) Kuti munthu uthawe ukagwidwa umafunika kuchita masamu. Chita mbera: Chita manyazi. Chitsanzo: Anthuwo atayamba kumuwowoza, anachita mbera. Chita milandu: Kukana mlandu. Chitsanzo: Mwana wawo ataba anayamba kuchita milandu. Chita ndukutu: Chita manyazi. Chitsanzo: Anthuwo atayamba kumuwowoza, anachita ndikutu. Chita nguma: Kakana. Chitsanzo: Mkazi uja nditamufunsira dzulo, anachita nguma. Chitanda: Mtembo. Chitsanzo: (1) Adzukulu anyamula chitanda. (2) Ndakumana nawo atanyamula chitanda. Chithangasala: Chisakasa chimangidwa ndi udzu kapena mapepala. Chitsanzo: Pamalo paja amangapo chithangasala. Chithunzithunzi: (a) Kufotokozera munthu zinthu zoti zimuthandize kuzindikira zinazake. Chitsanzo: Ndakufotokozerani zimenezi kuti ndikupatseni 42