Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 409

Bonwell “Kadyankena” Rodgers Pali anthu ena omwe amachititsa chidwi ponyadira chinenero chawo. Iwo amaluka komanso kukazingira chinenero chawo ndi nsinjiro za chiyankhulo komanso mawu apatali. Amaluka mawu okhetsa dovu, okhathamira ndi nsinjiro komanso ochititsa makutu kumva kuzuna kwa chiyankhulo. Koma n’zomvetsa chisoni kuti masiku ano ambiri akukankhira kumbali chinenero chathu cha Chichewa n’kumasonkhezera zinenero za mayiko ena. Chimenenechi ndi chizindikiro choti kupanda kusamala Chichewa chikhoza kutsenjira.