Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 407
Paphata pa Chichewa
zimakhala zozizira.
Zoziziritsa kukhosi (kum’mero): Chakumwa
chokhazikitsa mtima pansi, zakumwa zopha ludzu.
Chitsanzo: Ukatopa ndi dzuwa umafunika kudzipepesa
pogula zakumwa zoziziritsa kukhosi.
Zoziziritsa thupi: Nkhani zofooketsa, zochititsa mantha
kapena manyazi.
Chitsanzo: Zimene mwana ameneyu wachita ndi
zoziziritsa thupi.
Zozwetetsa mutu: Zosokoneza maganizo.
Chitsanzo: Mavuto ndikukumana nawo ine ndi ozwetetsa
mutu.
Zukuta: Kuyang’anitsitsa chinthu kuti upezepo chifukwa,
kukambirana mozama.
Chitsanzo: Tiyeni tizukute nkhaniyi bwinobwino.
Zula mano: Khaulitsa koopsa.
Chitsanzo: Mukawatengera maso m’mwamba
adzakuzulani mano.
Zula mnzako minga yapamsana: Kuthandiza munthu.
Minga yapansana imakhala yovuta kuzula chifukwa
mkono sungafikepo. Choncho kuzula munthu wina minga
ya pamsana ndi kumuthandiza kwambiri.
Chitsanzo: Amene aja ndi amene anandizula minga
yapansana.
Zungulira ngati nguli: Kuzungulirazungulira.
Chitsanzo: Osewera ena akamafuna kudyetsa njomva
amazungulira ngati nguli.
Zunguza lirime: Kugwiritsa ntchito lilime mochenjera.
Chitsanzo: Pulezidenti uyu yekha ndiye amadziwa
kuzunguza lirime.
Zunguza mutu: Kusokoneza mutu.
Chitsanzo: Samuyi ndi yozunguza mutu.
406