Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 404

Paphata pa Chichewa (b) Kudana ndi muthu. Chitsanzo: Amene aja amandizonda. Zonga: Kudula nyama mwadongosolo. Chitsanzo: (1) Muzonge nyamayi. (2) Muidule mizongomizongo. Zopanda ndi mchere womwe: Zopanda nzeru. Chitsanzo: Anabwera kunoko n’kumandiuza zopanda ndi mchere womwe! Zopanda pake: Zopanda nzeru, zosathandiza. Chitsanzo: Anangoona kukhala ndi imvi koma amangoyankhula zopanda pake. Zophwathalala: Zafulati, zophwanyika. Chitsanzo: Njerwa zake ndi zophwathalala. Zopola: Zosagwira mtima kwenikweni, zopanda nzeru, zosathandiza, zopanda mphamvu. Chitsanzo: Nthawi zonse nkhani zimene amakamba zimakhala zopola. Zopusa: (a) Zopanda nzeru. Chitsanzo: Ukuyankhulazi ndi zopusa. (b) Kugonana. Chitsanzo: Anawapeza akupanga zopusa. Zosakhala bwino: (1) Zosasangalatsa. Chitsanzo: Zimene zikuchitikazi ndi zosakhala bwino. (2) Zosakoma. Chitsanzo: Zakudya zakezi ndi zosakhala bwino. Zosakhala bwino: Zosasangalatsa kuzimva, zoipa. Chitsanzo: Nkhani zimene amandiuza ndi zosakhala bwino. Zosamveka: Zopanda mnzeru, zosathandiza. Chitsanzo: Ine ndikuona kuti zimene anenazo ndi 403