Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 401

Paphata pa Chichewa Zingalumephulan’tenga: Munthu wolimba mtima. Chitsanzo: (1) Ofula uchi amafunika kukhala zingalumephulan’tenga. (2) Munthu amene akufuna kuti zimuyendere amafunika kukhala zingalumephulan’tenga. Zingwa: Kusokonezeka, kudabwa. Chitsanzo: Mphalapalayo ataipanikiza inazigwa n’kulumphira m’dzenje. Zingwinjiri: Ndalama zachitsulo, zasiliva kapena golide. Chitsanzo: Angondipatsa zingwinjiri. Zinthu zapamwamba: Zinthu zodula, zabwino kwambiri. Chitsanzo: Amafuna zinthu zapamwamba. Zinyalala: Zinthu zotha ntchito kapena zosafunika. Chitsanzo: Apa ndi pamene amataya zinyalala. Zisamalidwe: (a) Zisatayike, zisawonongeke. Chitsanzo: Katundu uyu asamalidwe. (b) Kuba, kapena kutenga zinthu. Chitsanzo: Ndi ndani amene wasamala katundu wanga uja? Zisudzo: Nthabwala, sewero loseketsa anthu. Chitsanzo: Munthu ameneyu amapanga zisudzo. Zitsiru: Anthu opusa. Chitsanzo: Pakhomo pakachuluka zitsiru, mkamwini ndi amene amalamulira. Zivute zitani: Palibe chingandiletse. Chitsanzo: Sindisiya kugulitsa mang’ina zivute zitani. Ziwengo: Zipere. Chitsanzo: Usamayandikire anthu amene ali ndi ziwengo. Ziyenda: Zitheka, zikhala bwino. Chitanzo: Mukapitirizabe kuchita zinthu molimba mtima Ziyenda. 400