Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 400

Paphata pa Chichewa Zikuyenda? Zili bwino. Chitsanzo: Ife zili bwino, kaya anzathu bwanji, zikuyenda? Zilope: Mawuwa amanena za munthu amene akuchita zinthu mwamphamvu kwambiri ndipo sakufuna kusiya. Chitsanzo: Amagwira ntchito ngati ali ndi zilope. Zilubwelubwe: Kuona zinthu zomwe palibe. Chitsanzo: Nditangodzuka ndimaona zilubwelubwe. Zilumika: (a) Zaka. Chitsanzo: Papita zilumika zambiri chilandilireni ufulu. (b) Mawuwa amanenedwanso mokokomeza ponena za chinthu chikachedwa. Chitsanzo: Amati akapita kunsika amatengako zilumika. Zimandifikapo: Zimandisangalatsa kwambiri. Chitsanzo: Nyimbo zachikondi zimandifikapo. Zimbaitsa: Kunena mokuluwika, kunyalanyaza kunena mfundo yeniyeni. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani akunena mozimbaitsa. Zimbwatha: (a) Nkhuku ya miyendo yaifupi. Chitsanzo: Sindikufuna kuweta azimbwatha. (b) Munthu wamfupi. Chitsanzo: Abale ake onse ndi azimbwatha. Zimbwazimbwa: Saonekanso bwino. Chitsanzo: Poyamba ankatchena, koma pano amangoti zimbwazimbwa. Zina kambu zina leku: Ndi bwino kumaona zoyenera kunena m’malo momangoyankhula zilizonse. Chitsanzo: Zina kambu zina leku, mwanayu akuchita bwino zedi! Zinamwa njuchi: Mwamuna wosabereka. Chitsanzo: Bambowatu alibe mwana, zinamwa njuchi. 399