Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 40

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Ataona kuti anzawo agula galimoto, nawonso anakagula chiphapha chawo. Chipheradzuwa: Mowa wolawa. Chitsanzo: Akufuna muwapatse kaye chipheradzuwa. Chiphuphamoyo: Kuvutika mumtima. Chitsanzo: (1) Nditamva zoti akuvutika m’thupi, ndinagona mwa chiphuphamoyo. (2) Ndikudwala moti ndikungoyendera chiphuphamoyo. Chiphuphu: (a) Kupereka ndalama n’cholinga choti akukondere kapena akuchitire chinachake chomwe samafunika kukuchitira. Chitsanzo: Anthu ambiri a m’boma amachita ziphuphu. (b) Zilonda za pankhope. Chitsanzo: Mwana akamakula amayamba ziphuphu. Chipondam’thengo: Ndalama kapena chinachake chomwe munthu amapereka kwa sing’anga asanapite kukafuna mankhwala. Chitsanzo: Mukamapita musaiwale kutenga kandalama chifukwa ng’anga yake singakakuthandizeni popanda kuipatsa chiponda mthengo. Chipsinjo: (a) Wosamva. Chitsanzo: Mwana uyu ndi chipsinjo. (b) Mavuto. Chitsanzo: Anzanu aja ali pachipsinjo. Chipsolopsolo: Mnyamata. Mawuna amatanthauzanso tambala yemwe wangoyamba kumene kulira. 39